Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Estere 5:12-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. Hamani anatinso, Ndiponso Estere mkazi wamkuru sanalola mmodzi yense alowe pamodzi ndi mfumu ku madyerero adakonzawo, koma ine ndekha; nandiitana mawanso pamodzi ndi mfumu.

13. Koma zonsezi sindipindula nazo kanthu konse, pokhala ndirikuona Moredekai Myudayo alikukhala ku cipata ca mfumu.

14. Pamenepo Zeresi mkazi wace, ndi mabwenzi ace onse ananena naye, Apange mtengo, msinkhu wace mikono makumi asanu, ndi mawa mukanene nayo mfumu kuti ampacike Moredekai pamenepo; nimulowe pamodzi ndi mfumu kumadyerero wokondwera. Ndipo ici cidakomera Hamani, napangitsa anthu mtengowo.

Werengani mutu wathunthu Estere 5