Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Estere 4:14-17 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

14. Pakuti ukakhala cete konse tsopano lino, cithandizo ndi cipulumutso zidzafuma kwina; koma iwe ndi nyumba ya atate wako mudzaonongeka; ndipo kaya, kapena walowera ufumu cifukwa ca nyengo yonga iyi.

15. Pamenepo Estere anati ambwezere mau Moredekai,

16. Muka, sonkhanitsa Ayuda onse opezeka m'Susani, nimundisalire, osadya osamwa masiku atatu, usiku ndi usana, ine ndemwe ndi anamwali anga tidzasala momwemo, ndipo motero ndidzalowa kwa mfumu, ndiko kosalingana ndi lamulo; ndikaonongeka tsono ndionongeke,

17. Napita Moredekai, nacita monga mwa zonse adamlamulira Estere.

Werengani mutu wathunthu Estere 4