Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Estere 4:1-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Koma podziwa Moredekai zonse zidacitikazi, Moredekai anang'amba zobvala zace, nabvala ciguduli ndi mapulusa, naturuka pakati pa mudzi, napfuula, nalira kulira kwakukuru ndi kowawa,

2. nafika popenyana ndi cipata ca mfumu; popeza sanathe munthu kulowa ku cipata ca mfumu wobvala ciguduli.

3. Ndi m'maiko monse, pali ponse anafikapo mau a mfumu ndi lamulo lace, panali maliro akuru mwa Ayuda, ndi kusala, ndi kulira misozi, ndi kubuma; nagona m'ciguduli ndi mapulusa ambiri.

4. Ndipo anamwali a Estere ndi adindo ace anadza, namuuza; ndi mkazi wamkuru anawawidwa mtima kwambiri, natumiza cobvala abveke Moredekai, ndi kumcotsera ciguduli cace; koma sanacilandira.

5. Pamenepo Estere anaitana Hataki mdindo wina wa mfumu, amene idamuika amtumikire, namuuza amuke kwa Moredekai, kuti adziwe ici nciani ndi cifukwa cace ninji.

6. Naturuka Hataki kumka kwa Moredekai ku khwalala la mudzi linali popenyana ndi cipata ca mfumu.

7. Ndipo Moredekai anamfotokozera zonse zidamgwera, ndi mtengo wace wa ndarama adati Hamani adzapereka m'nyumba ya cuma ca mfumu pa Ayuda, kuwaononga.

8. Anampatsanso citsanzo ca lamulo lolembedwa adalibukitsa m'Susani, kuwaononga, acionetse kwa Estere, ndi kumfotokozera, ndi kumlangiza alowe kwa mfumu, kumpembedza, ndi kupempherera anthu ace kwa iye.

9. Nadza Hataki, namuuza Estere mau a Moredekai.

Werengani mutu wathunthu Estere 4