Ndipo Moredekai anamfotokozera zonse zidamgwera, ndi mtengo wace wa ndarama adati Hamani adzapereka m'nyumba ya cuma ca mfumu pa Ayuda, kuwaononga.