Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Estere 3:4-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

4. Kunali tsono, pomalankhula naye tsiku ndi tsiku, osawamvera iye, anauza Hamani, kuona ngati mlandu wa Moredekai udzakoma; popeza iye adawauza kuti ali Myuda.

5. Ndipo Hamani, pakuona kuti Moredekai sanamweramira kapena kumgwadira, mtima wace unadzala mkwiyo.

6. Koma anaciyesa copepuka kumthira manja Moredekai yekha; pakuti adamfotokozera mtundu wace wa Moredekai; potero Hamani anafuna kuononga Ayuda lonse okhala m'ufumu wonse wa Ahaswero, ndiwo a mtundu wa Moredekai.

7. Mwezi woyamba ndiwo mwezi wa Nisani, caka cakhumi ndi ciwiri ca mfumu Ahaswero, anaombeza Puri, ndiwo ula, pamaso pa Hamani tsiku ndi tsiku, mwezi ndi mwezi, mpaka mwezi wakhumi ndi ciwiri, ndiwo mwezi wa Adara.

8. Ndipo Hamani anati kwa mfumu Ahaswero, Pali mtundu wina wa anthu obalalika ndi ogawanikana mwa mitundu ya anthu m'maiko onse a ufumu wanu, ndi malamulo ao asiyana nao a anthu onse, ndipo sasunga malamulo a mfumu; cifukwa cace mfumu siiyenera kuwaleka.

9. Cikakomera mfumu, cilembedwe kuti aonongeke iwo; ndipo ndidzapereka matalente a siliva zikwi khumi m'manja a iwo akusunga nchito ya mfumu, abwere nao kuwaika m'nyumba za cuma ca mfumu.

10. Ndipo mfumu inabvula mphete yace pa cala cace, naipereka kwa Hamani mwana wa Hamedata wa ku Agagi, mdani wa Ayuda.

11. Ndipo mfumu idati kwa Hamani, Siliva akhale wako, ndi anthu omwe; ucite nao monga momwe cikukomera.

Werengani mutu wathunthu Estere 3