Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Estere 2:16-22 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

16. Momwemo anatengedwa Estere kumka kwa mfumu Ahaswero, ku nyumba yace yacifumu, mwezi wakhumi, ndiwo mwezi wa Tebete, caka cacisanu ndi ciwiri ca ufumu wace.

17. Ndipo mfumu inakonda Estere koposa akazi onse, nalandira iye kuyanja ndi cifundo pamaso pace, koposa anamwali onse; motero anaika korona wacifumu pamutu pace, namuyesa mkazi wamkuru m'malo mwa Vasiti.

18. Pamenepo mfumu inawakonzera madyerero akuru ace onse, ndi omtumikira, ndiwo madyerero a Estere; napumulitsa maiko, naninkha zaufulu monga mwa ufulu wa mfumu.

19. Ndipo posonkhanidwa anamwali nthawi yaciwiri Moredekai anali wa m'bwalo la mfumu.

20. Estere sadaulula cibale cace kapena mtundu wace, monga Moredekai adamuuza; popeza Estere anacita mau a Moredekai monga m'mene analeredwa naye.

21. Masiku awa pokhala Moredekai wa m'bwalo la mfumu, Bigitana ndi Teresi, adindo awiri a mfumu osunga pakhomo, anapsa mtima, nayesa kumthira manja mfumu Ahaswero.

22. Koma cidadziwika ici kwa Moredekai, ndiye anafotokozera Estere mkazi wamkuru; ndi Estere anamuuza mfumu, kumnenera Moredekai.

Werengani mutu wathunthu Estere 2