Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Estere 2:1-6 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Zitatha izi, utaleka mkwiyo wa mfumu Ahaswero, anakumbukila Vasiti, ndi cocita iye, ndi comlamulidwira.

2. Pamenepo anyamata a mfumu omtumikira anati, Amfunire mfumu anamwali okongola;

3. ndi mfumu aike oyang'anira m'maiko onse a ufumu wace, kuti asonkhanitse anamwali onse okongola m'cinyumba ca ku Susani, m'nyumba ya akazi; awasunge Hege mdindo wa mfumu wosungira akazi, nawapatse zowayeretsa;

4. ndi namwali womkonda mfumu akhale mkazi wamkuru m'malo mwa Vasiti. Ndipo cinthuci cinamkonda mfumu, nacita comweco.

5. Panali Myuda m'cinyumba ca ku Susani, dzina lace ndiye Moredekai, mwana wa Yairi, mwana wa Simei, mwana wa Kisi Mbenjamini;

6. uyu anatengedwa ndende ku Yerusalemu, pamodzi ndi andende anatengedwa pamodzi ndi Yekoniya mfumu ya Yuda, amene Nebukadinezara mfumu ya Babulo adamtenga ndende.

Werengani mutu wathunthu Estere 2