Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Eksodo 7:3-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

3. Koma Ine ndidzaumitsa mtima wace wa Farao, ndipo ndidzacurukitsa zizindikilo ndi zozizwa zanga m'dziko la Aigupto.

4. Koma Farao sadzamvera inu, ndipo ndidzaika dzanja langa pa Aigupto, ndipo ndidzaturutsa makamu anga, anthu anga ana a Israyeli, m'dziko la Aigupto ndi maweruzo akuru.

5. Ndipo Aaigupto adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, pakutambasula Ine dzanja langa pa Aigupto, ndi kuturutsa ana a Israyeli pakati pao.

6. Ndipo Mose ndi Aroni anacita monga Yehova anawalamulira, momwemo anacita.

7. Ndipo Mose anali nazo zaka makumi asanu ndi atatu, ndi Aroni anali nazo zaka makumi asanu ndi atatu kudza zitatu, pamene ananena ndi Farao.

8. Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi Aroni, ndi kuti,

9. Pamene Farao adzalankhula nanu, ndi kuti, Dzicitireni codabwiza; pamenepo uzinena ndi Aroni, Tenga ndodo yako, Iponye pansi pamaso pa Farao, isanduke cinjoka,

10. Ndipo Mose ndi Aroni analowa kwa Farao, nacita monga momwe Yehova adawalamulira; ndipo Aroni anaponya pansi ndodo yace pamaso pa Farao, ndi pamaso pa anyamata ace, ndipo inasanduka cinjoka,

11. Pamenepo Farao anaitananso anzeru, ndi amatsenga; ndipo alembi a Aigupto, iwonso anacita momwemo ndi matsenga ao.

12. Pakuti yense anaponya pansi ndodo yace, ndipo zinasanduka zinjoka; koma ndodoya Aroni inameza ndodo zao,

13. Koma mtima wa Farao unalimba, ndipo sanamvera iwo; monga adalankhula Yehova.

14. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, Walemera mtima wa Farao, akana kulola anthu apite,

15. Muka kwa Farao m'mawa; taona, aturuka kumka kumadzi; nuime kumlinda m'mbali mwa nyanja; ndi ndodo idasanduka njokayo uigwire m'dzanja lako.

16. Ndipo ukanena naye, Yehova, Mulungu wa Ahebri anandituma kwa inu, ndi kuti, Lola anthu anga amuke kuti anditumukire m'cipululu; koma, taona, sunamvera ndi pano.

Werengani mutu wathunthu Eksodo 7