Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Eksodo 7:20-25 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

20. Ndipo Mose ndi Aroni anacita monga momwe Yehova adawalamulira; nasamula ndodo, napanda madzi ali m'nyanjamo pamaso pa Farao, ndi pamaso pa anyamata ace; ndipo madzi onse a m'nyanjamo anasanduka mwazi.

21. Ndi nsomba za m'nyanjamo zinafa; ndi nyanjayo inanunkha; ndipo Aaigupto sanakhoza kumwa madzi a m'nyanjamo; ndipo munali mwazi m'dziko lonse la Aigupto.

22. Ndipo alembi a Aigupto anacita momwemo ndi matsenga ao; koma mtima wa Farao unalimba, ndipo sanamvera iwo; monga adalankhula Yehova.

23. Ndipo Farao anatembenuka, nalowa m'nyumba yace, osasamalira ici comwe mumtima mwace.

24. Koma Aaigupto onse anakumba m'mphepete mwa nyanja kufuna madzi akumwa; pakuti sanakhoza kumwa madzi a m'nyanjamo.

25. Ndipo anafikiramasiku asanu ndi awiri atapanda nyanja Yehova.

Werengani mutu wathunthu Eksodo 7