Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Eksodo 7:11-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

11. Pamenepo Farao anaitananso anzeru, ndi amatsenga; ndipo alembi a Aigupto, iwonso anacita momwemo ndi matsenga ao.

12. Pakuti yense anaponya pansi ndodo yace, ndipo zinasanduka zinjoka; koma ndodoya Aroni inameza ndodo zao,

13. Koma mtima wa Farao unalimba, ndipo sanamvera iwo; monga adalankhula Yehova.

14. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, Walemera mtima wa Farao, akana kulola anthu apite,

15. Muka kwa Farao m'mawa; taona, aturuka kumka kumadzi; nuime kumlinda m'mbali mwa nyanja; ndi ndodo idasanduka njokayo uigwire m'dzanja lako.

16. Ndipo ukanena naye, Yehova, Mulungu wa Ahebri anandituma kwa inu, ndi kuti, Lola anthu anga amuke kuti anditumukire m'cipululu; koma, taona, sunamvera ndi pano.

17. Atero Yehova, Ndi ici udzadziwa kuti Ine ndine Yehova: taonani, ndidzapanda madzi ali m'nyanja ndi ndodo iri m'dzanja langa, ndipo adzasanduka mwazi.

18. Ndi nsomba ziri m'nyanja zidzafa, ndi nyanja idzanunkha; ndi Aaigupto adzacita mtima useru ndi kumwa madzi a m'nyanjamo.

Werengani mutu wathunthu Eksodo 7