19. Ndipo ana amuna a Merai ndiwo: Mali ndi Musi. Amenewo ndiwo mabanja a Levi mwa kubadwa kwao.
20. Ndipo Amramu anadzitengera Yokobedi mlongo wa atate wace akhale mkazi wace; ndipo anambalira Aroni ndi Mose; ndi zaka za moyo wa Amramu ndizo zaria limodzi mphambu makumi atatu kudza zisanu ndi ziwiri.
21. Ndi ana amuna a lzara ndiwo: Kora: ndi Nefegi, ndi Zikiri.
22. Ndi ana amuna a Uziyeli ndiwo: Misayeli, ndi Elisafana, ndi Sitiri.
23. Ndipo Aroni anadzitengera Eliseba, mwana wamkazi wa Aminadabu, mlongo wace wa Nasoni, akhale mkazi wace; ndipo anambalira Nadabu ndi Abihu, Eleazara ndi ltamara.
24. Ndipo ana amuna a Kora ndiwo: Asiri ndi Elikana, ndi Abiasafu; amenewo ndiwo mabanja a Akora.
25. Ndipo Eleazara mwana wa Aroni anadzitengera mkazi wa ana akazi a Putieli akhale mkazi wace, ndipo anambalira Pinehasi. Amenewo ndi akuru a makolo a Alevi mwa mabanja ao.