Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Eksodo 5:16-23 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

16. Udzu osawapatsa akapolo anu, ndipo amanena ndi ife, Umbani njerwa; ndipo, taonani, amapanda akapolo anu; koma kulakwa nkwa anthu anu.

17. Koma iye anati, Aulesi inu, aulesi: cifukwa cace mulikunena, Timuke, timphere nsembe Yehova.

18. Mukani tsopano, gwirani nchito; pakuti sadzakupatsani udzu, koma muonetse ciwerengero cace ca njerwa.

19. Ndipo akapitao a ana a Israyeli anaona kuti kudawaipira, pamene ananena, Musamacepetsa njerwa zanu, nchito ya tsiku pa tsiku lace.

20. Ndipo poturuka kwa Farao iwo anakomana ndi Mose ndi Aroni, alikuima popenyana nao;

21. ndipo ananena nao, Yehova akupenyeni, naweruze; pakuti mwatinyansitsa pamaso pa Farao, ndi pamaso pa anyamata ace, ndi kuwapatsa lupanga m'dzanja lao kutipha nalo.

22. Pamenepo Mose anabwerera namka kwa Yehova, nati, Ambuye, mwawacitiranji coipa anthuwa? mwandituma bwanji?

23. Popeza kuyambira kuja ndinafika kwa Farao kulankhula m'dzina lanu, anawacitira coipa anthuwa; ndipo simunalanditsa anthu anu konse.

Werengani mutu wathunthu Eksodo 5