Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Eksodo 5:1-4 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo pambuyo pace Mose ndi Aroni analowa nanena ndi Farao, Atero Yehova, Mulungu wa Israyeli, Lola anthu anga apite, kundicitira madyerero m'cipululu.

2. Koma Farao anati, Yehova ndani, kuti ndimvere mau ace ndi kulola Israyeli apite? Sindimdziwa Yehova, ndiponso sindidzalola Israyeli apite.

3. Ndipo iwo anati, Mulungu wa Ahebri wakomana ndi ife; timuketu ulendo wa masiku atatu m'cipululu, kumphera nsembe Yehova Mulungu wathu; kuti angatikumike ndi mliri, kapena ndi lupanga,

4. Ndipo mfumu ya Aigupto inanena nao, Inu, Mose ndi Aroni, cifukwa ninji mumasulira anthu nchito zao? Mukani ku akatundu anu.

Werengani mutu wathunthu Eksodo 5