Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Eksodo 39:32-43 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

32. Potero anatsiriza nchito yonseya kacisi wa cihema cokomanako; ndipo ana a Israyeli adacita monga mwa zonse Yehova adamuuza Mose, anacita momwemo.

33. Ndipo anabwera naye kacisi kwa Mose, cihemaco, ndi zipangizo zace zonse, zokowera zace, matabwa ace, mitanda yace, ndi mizati yace, nsanamira zace ndi nsici zace, ndi makamwa ace;

34. ndi cophimba ca zikopa za nkhosa zamphongo zonika zofiirira, ndi cophimba ca zikopa za akatumbu, ndi nsaru yocinga yotsekera;

35. likasa la mboni, ndi mphiko zace, ndi cotetezerapo;

36. gomelo, zipangizo zace zonse, ndi mkate woonekera;

37. coikapo nyali coona, nyali zace, ndizo nyali zimakonzekazi, ndi zipangizo zace zonse, ndi mafuta a kuunikira;

38. ndi guwa la nsembe lagolidi, ndi mafuta odzoza, ndi cofukiza ca pfungo lokoma, ndi nsaru yotsekera pa khomo la cihemaco;

39. guwa la nsembe lamkuwa, ndi made ace amkuwa, mphiko zace, ndi zipangizo zace zonse, mkhate ndi tsinde lace;

40. nsaru zocingira za pabwalo, osici zace, ndi makamwa ace, ndi nsaru yotsekera pa cipata ca pabwalo, zingwe zace, ndi ziciri zace, ndi zipangizo zonse za nchito ya kacisi, za ku cihema cokomanako;

41. zobvala zokoma za kutumikira nazo m'malo opatulika, ndi zobvala zopatulika za Aroni wansembe, ndi zobvala za ana ace, kucita nazo nchito ya usembe.

42. Monga mwa zonse Yehova adamuuza Mose, momwemo ana a Israyeli anacita nchito zonse.

43. Ndipo Mose anaona nchito zonse, ndipo, taonani, adaicita monga Yehova adamuuza, momwemo adacita. Ndipo Mose anawadalitsa.

Werengani mutu wathunthu Eksodo 39