Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Eksodo 39:18-28 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

18. Ndi nsonga zace ziwiri zina za maunyolo awiri opotawo anazimanga pa zoikamo ziwiri, nazimanga pa zapamapewa za efodi, m'tsogolo mwace.

19. Ndipo anapanga mphete ziwiri zagolidi, naziika pa nsonga ziwiri za capacifuwa, m'mphepete mwace m'katimo, pa mbali ya kuefodi.

20. Ndipo anapanga mphete ziwiri zagolidi, naziika pa zapamapewa ziwiri za efodi pansi pace, pa mbali yace ya kutsogolo, pafupi pa msoko wace, pamwamba pa mpango wa efodi.

21. Ndipo anamanga capacifuwa pa mphete zace ndi mphete za efodi ndi mkuzi wamadzi, kuti cikhale pa mpango wa efodi, ndi kuti capacifuwa cisamasuke paefodi; monga Yehova anamuuza Mose.

22. Ndipo anaomba mwinjiro wa efodi, nchito yoomba ya lamadzi lokha;

23. ndi pakati pace polowa mutu, ngati polowa pa maraya ocingirizira, ndipo anabinyira pozungulira polowa pace, pangang'ambike.

24. Napangira pa mkawo wa mwinjiro makangaza a lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa.

25. Ndipo anapanga miriu ya golidi woona, napakiza miriu ndi makangaza, pa mkawo wa mwinjiro pozungulira, popakiza ndi makangaza.

26. Mliu ndi khangaza, mliu ndi khangaza pa mkawo wa mwinjiro pozungulira, kutumikira nazo; monga Yehova anamuuza Mose.

27. Ndipo anaomba maraya a bafuta, a nchito yoomba, a Aroni, ndi a ana ace amuna,

28. ndi nduwira va bafuta wa thonje losansitsa, ndi akapal okometsetsa a bafuta wa thonje losansitsa, ndi zobvala za kumiyendo za bafuta wa thonje losansitsa,

Werengani mutu wathunthu Eksodo 39