Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Eksodo 39:1-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo anaomba zobvala zakutumikira nazo ndi lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, atumikire nazo m'malo opatulika, naomba zobvala zopatulika za Aroni; monga Yehova adamuuza Mose.

2. Ndipo anaomba efodi wa golidi, lamadzi, lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa.

3. Ndipo anasula golidi waphanthiphanthi, nalemba nsambo, kuti amuombe pamodzi ndi lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa, nchito ya mmisiri.

4. Anapangira efodi zapamapewa zolumikizana; pa nsonga ziwirizo anamlumikiza.

5. Ndi mpango wa efodi wokhala pamenepo, wakummanga nao unali woombera kumodzi wa ciombedwe comweci; wa golidi, ndi lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa; monga Yehova adauza Mose.

6. Ndipo anakonza miyala yasohamu, yogwirika m'zoikamo zagolidi, yoloca ngati malocedwe a cosindikizira, ndi maina a ana a lsrayeli.

7. Ndipo anaiika pa zapamapewa za efodi, ikhale miyala ya cikumbutso kwa ana a Israyeli; monga Yehova adamuuza Mose.

8. Ndipo anaomba capacifuwa, nchito ya mmisiri, monga maombedwe ace a efodi; ca golidi, lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa.

9. Cinakhala camowamphwa; anaciomba capacifuwa copindika; utali wace cikhato cimodzi, ndi kupingasa kwace cikhato cimodzi, cinakhala copindika.

10. Ndipo anaika pomwepo mizere inai ya miyala; mzere wa odemu, pitida, ndi bareketi, ndiyo ya mzere woyamba.

Werengani mutu wathunthu Eksodo 39