Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Eksodo 37:1-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo Bezaleli anapanga likasa la mtengo wasitimu; utali wace mikono iwiri ndi hafu, ndi kupingasa kwace mkono ndi hafu, ndi msinkhu wace mkono ndi hafu;

2. ndipo analikuta ndi golidi woona m'kati ndi kunja, nalipangira mkombero wagolidi pozungulira pace.

3. Ndipo analiyengera mphete zinai zagolidi pa miyendo yace inai; mphete ziwiri pa mbali yace imodzi, ndi mphete: ziwiri pa mbali yace yina.

4. Ndipo anapanga mphiko za mtengo wasitimu, nazikuta ndi golidi.

5. Ndipo anapisa mphiko m'mphetezo pa mbali zace za likasalo, kuti anyamulire nazo likasa.

6. Ndipo anapanga cotetezerapo ca golidi woona; utali wace mikono iwiri ndi hafu, ndi kupingasa kwace mkono ndi hafu.

7. Anapanganso akerubi awiri agolidi; anacita kuwasula mapangidwe ace, pa mathungo ace swiri a coteteze rapo;

8. kerubi mmodzi pa mbali yace imodzi, ndi kerubi wilia pa mbali yace yina; anapanga akerubi ocokera m'cotetezerapo, pa mathungo ace awiri.

9. Ndipo akerubi anafunyulira mapiko ao m'mwamba, ndi kuphimba cotetezerapo ndi mao piko ao, ndi nkhope zao zopeoyana; zinapenya kucotetezerapo nkhope zao.

Werengani mutu wathunthu Eksodo 37