Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Eksodo 33:8-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

8. Ndipo kunali, pakuturuka Mose kumka ku cihemaco kuti anthu onse anaimirira, nakhala ciriri, munthu yense pakhomo pa hema wace, nacita cidwi pa Mose, kufikira atalowa m'cihemaco.

9. Ndipo kunali, pakulowa Mose m'cihemaco, mtambo njo udafutsika, nuima pakhomo pa cihemaco; ndipo Yehova analankhula ndi Mose.

10. Ndipo anthu onse anaona mtambo njo ulikuima pakhomo pa cihema; ndi anthu onse anaimirira, nalambira, yense pakhomo pa hema wace.

11. Ndipo Yehova ananena ndi Mose kopenyana maso, monga munthu alankhula ndi bwenzi lace. Ndipo anabwerera kumka kucigono; koma mtumiki wace Yoswa, mwana wa Nuni, ndiye mnyamata msinkhu wace, sanacoka m'cihemamo.

12. Ndipo Mose anati kwa Yehova, Taonani, Inu munena ndi ine, Kwera nao anthu awa; koma simunandidziwitsa amene mudzamtuma amuke nane. Koma munati, Ndikudziwa dzina lako, wapezanso ufulu pamaso panga,

13. Ndipo tsopano, ngati ndapeza ufulu pamaso panu, mundidziwitsetu njira zanu, kuti ndikudziweni, ndi kuti ndipeze ufulu pamaso panu; ndipo penyani kuti mtundu uwu ndi anthu anu.

14. Ndipo anati, Nkhope yanga idzamuka nawe, ndipo ndidzakupumuza.

15. Ndipo ananena ndi Iye, Ikapanda kumuka nane nkhope yanu, musatikweze kucokera kuno.

16. Pakuti cidziwfka ndi ciani tsopano kuti ndapeza ufulu pamaso panu, ine ndi anthu anu? Si pakumuka nafe Inu, kuti ine ndi anthu anu tisiyane ndi anthu onse akukhala pa nkhope ya dziko lapansi?

Werengani mutu wathunthu Eksodo 33