Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Eksodo 33:1-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo Yehova anati kwa Mose, Muka, kwera kucokera kuno, iwe ndi anthu amene unawakweza kucokera m'dziko la Aigupto, kumka ku dzikolo ndinalumbirira nalo Abrahamu, ndi Isake, ndi Yakobo, ndi kuti, Ndidzapatsa mbeu zako ilo;

2. ndipo ndidzatuma mthenga akutsogolere; ndipo ndidzapitikitsa Akanani, ndi Aamori, ndi Ahiti, ndi Aperizi, Ahivi, ndi Ayebusi;

3. kudziko koyenda mkaka ndi uci ngati madzi; pakuti sindidzakwera pakati pa inu; popeza inu ndinu anthu opulupudza; ndingathe inu panjira.

4. Ndipo pamene anthu anamva mau awa oipa anacita cisoni; ndipo panalibe mmodzi anabvala zokometsera zace.

5. Ndipo Yehova anati kwa Mose, Nena ndi ana a Israyeli, Inu ndinu anthu opulupudza; ndikakwera kulowa pakati pa inu kamphindi kamadzi, ndidzakuthani; koma tsopano, bvulani zokometsera zanu, kuti ndidziwe comwe ndikucitireni.

6. Ndipo ana a Israyeli anazicotsera zokometsera zao kuyambira pa phiri la Horebe.

7. Ndipo Mose akatenga cihemaco nacimanga kunja kwa cigono, kutari kwa cigono; nacicha, Cihema cokomanako. Ndipo kunakhala kuti yense wakufuna Yehova anaturuka kumka ku cihema cokomanako kunja kwa cigono.

8. Ndipo kunali, pakuturuka Mose kumka ku cihemaco kuti anthu onse anaimirira, nakhala ciriri, munthu yense pakhomo pa hema wace, nacita cidwi pa Mose, kufikira atalowa m'cihemaco.

9. Ndipo kunali, pakulowa Mose m'cihemaco, mtambo njo udafutsika, nuima pakhomo pa cihemaco; ndipo Yehova analankhula ndi Mose.

10. Ndipo anthu onse anaona mtambo njo ulikuima pakhomo pa cihema; ndi anthu onse anaimirira, nalambira, yense pakhomo pa hema wace.

11. Ndipo Yehova ananena ndi Mose kopenyana maso, monga munthu alankhula ndi bwenzi lace. Ndipo anabwerera kumka kucigono; koma mtumiki wace Yoswa, mwana wa Nuni, ndiye mnyamata msinkhu wace, sanacoka m'cihemamo.

12. Ndipo Mose anati kwa Yehova, Taonani, Inu munena ndi ine, Kwera nao anthu awa; koma simunandidziwitsa amene mudzamtuma amuke nane. Koma munati, Ndikudziwa dzina lako, wapezanso ufulu pamaso panga,

13. Ndipo tsopano, ngati ndapeza ufulu pamaso panu, mundidziwitsetu njira zanu, kuti ndikudziweni, ndi kuti ndipeze ufulu pamaso panu; ndipo penyani kuti mtundu uwu ndi anthu anu.

Werengani mutu wathunthu Eksodo 33