Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Eksodo 32:26-35 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

26. Mose anaima pa cipata ca cigono, nati, Onse akubvomereza Yehova, adze kwa ine. Pamenepo ana amuna onse a Levi anasonkhana kwa iye,

27. Ndipo ananena nao, Atero Yehova Mulungu wa Israyeli, Yense amange lupanga lace m'cuuno mwace, napite, nabwerere kuyambira cipata kufikira cipata, pakati pa cigono, naphe yense mbale wace, ndi yense bwenzi lace, ndi yense mnansi wace.

28. Ndipo ana a Levi anacita monga mwa mau a Mose; ndipo adagwa tsiku lija anthu ngati zikwi zitatu.

29. Popeza Mose adati, Mdzazireni Yehova manja anu lero, pakuti yense akhale mdani wa mwana wace wamwamuna, ndi mdani wa mbale wace; kuti akudalitseni lero lino.

30. Ndipo kunali m'mawa mwace, kuti Mose anati kwa anthu, Mwacimwa kucimwa kwakukulu; koma ndikwera kwa Yehova tsopano, kapena ndidzacita cotetezera ucimo wanu.

31. Ndipo Mose anabwerera kumka kwa Yehova, nati, Ha! pepani, anthu awa anacimwa kucimwa kwakukuru, nadzipangira milungu yagolidi.

32. Koma tsopano, kapena mudzakhululukira kucimwa kwao; koma ngati mukana, mundifafanizetu, kundicotsa m'buku lanu limene munalembera,

33. Ndipo Yehova anati kwa Mose, iye amene wandicimwira, ndifafaniza yemweyo kumcotsa m'buku langa.

34. Ndipo tsopano, muka, tsogolera anthu kumka nao kumene ndinakuuza; taona, mthenga wanga akutsogolera; koma tsiku lakuwazonda Ine ndidzawalanga cifukwa ca kucimwa kwao.

35. Ndipo Yehova anakantha anthu, cifukwa anapanga mwana wa ng'ombe amene Aroni anapanga.

Werengani mutu wathunthu Eksodo 32