Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Eksodo 32:20-26 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

20. Ndipo anatenga mwana wa ng'ombe anampangayo, namtentha ndi moto, nampera asalale, namwaza pamadzi, namwetsako ana a Israyeli.

21. Ndipo Mose anati kwa Aroni, Anthu awa anakucitiranji, kuti iwe watengera iwo kulakwa kwakukuru kotere?

22. Ndipo Aroni anati, Asapse mtima mbuye wanga; udziwa anthuwa kuti akhumba coipa.

23. Pakuti ananena nane, Tipangireni milungu yakutitsogolera; popeza Mose uyu, munthuyu anatikweza kucokera m'dziko la Aigupto, sitidziwa comwe camgwera.

24. Ndipo ndinanena nao, Ali yense ali naye golidi amthyole; ndipo anandipatsa; ndipo ndinaciponya m'moto, ndimo anaturukamo mwana wa ng'ombe uyu.

25. Ndipo pamene Mose anaona kuti anthu anamasuka, popeza Aroni adawamasula kuti awatonze adani ao,

26. Mose anaima pa cipata ca cigono, nati, Onse akubvomereza Yehova, adze kwa ine. Pamenepo ana amuna onse a Levi anasonkhana kwa iye,

Werengani mutu wathunthu Eksodo 32