Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Eksodo 29:40-46 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

40. ndi pa mwana wa nkhosa mmodziyo pakhale limodzi la magawo khumi la ufa wosalala, wosanganiza ndi limodzi la magawo anai la hini wa mafuta opera; ndi limodzi la magawo anai la hini wa vinyo, likhale nsembe yothira.

41. Ndi mwana wa nkhosa wina ukonze madzulo; umkonze umo unacitira copereka ca m'mawa ndi nsembe yace yothira, akhale pfungo lokoma, nsembe yamoto ya Yehova.

42. Ikhale nsembe yopsereza yosalekeza ya mwa mibadwo yanu, pa khomo la cihema cokomanako, pamaso pa Yehova, kumene ndidzakomana nanu, kulankhula nawe komweko.

43. Ndipo pamenepo ndidzakomana ndi ana a Israyeli; ndipo cihema cidzapatulidwa ndi ulemerero wanga.

44. Ndipo ndidzapatula cihema cokomanako, ndi guwa la nsembe; ndidzapatulanso Aroni ndi ana ace amuna omwe, andicitire nchito ya nsembe.

45. Ndipo ndidzakhala pakati pa ana a Israyeli, ndi kukhala Mulungu wao.

46. Ndipo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova Mulungu wao, amene ndinawaturutsa m'dziko la Aigupto, kuti ndikhale pakati pao. Ine ndine Yehova Mulungu wao.

Werengani mutu wathunthu Eksodo 29