Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Eksodo 29:11-20 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

11. Nuphe ng'ombe yamphongoyo pamaso pa Yehova, pa khomo la cihema cokomanako.

12. Pamenepo utapeko pa mwazi wa ng'ombe yamphongo, ndi kuupaka pa nyanga za guwa la nsembe ndi cala cako, nutsanulire mwazi wonse pa tsinde la guwa la nsembe.

13. Nutenge mafuta onse akukuta matumbo, ndi cokuta ca mphafa ndi imso ziwiri, ndi mafuta ali pa izo, ndi kuzitentha pa guwa la nsembe.

14. Koma nyama ya ng'ombeyo, ndi cikopa cace, ndi cipwidza cace, uzitentha izi ndi moto kunja kwa cigono; ndiyo nsembe yaucimo.

15. Utengenso nkhosa yamphongo imodziyo; ndi Aroni ndi ana ace amuna aike manja ao pamutu pa nkhosa yamphongoyo.

16. Nuiphe nkhosa yamphongoyo, ndi kutenga mwazi wace, ndi kuuwaza pa guwa la nsembe pozungulira.

17. Ndipo upadzule nkhosa yamphongo m'ziwalo zace, ndi kutsuka matumbo ace, ndi miyendo yace, ndi kuziika pa ziwalo zace, ndi pamutu pace.

18. Pamenepo upsereze, nkhosa yamphongo yonse pa guwa la nsembe; ndiyo nsembe yopsereza ya Yehova, ya pfungo lokoma; ndiyo nsembe yamoto ya Yehova.

19. Ndipo utenge nkhosa yamphongo yinayo; ndi Aroni ndi ana ace amuna aike manja ao pamutu pa nkhosa yamphongoyo.

20. Pamenepo uiphe nkhosa yamphongoyo, nutapeko pa mwazi wace, ndi kuupaka pa ndewerere ya khutu lamanja la Aroni, ndi pa ndewerere ya khutu lamanja la ana ace amuna, ndi pa cala cacikulu ca dzanja lao lamanja, ndi pa cala cacikulu ca phazi lao lamanja, ndi kuuwaza mwaziwo pa guwa la nsembe posungulira,

Werengani mutu wathunthu Eksodo 29