Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Eksodo 28:3-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

3. Ndipou lankhule ndi onse a mtima waluso, amene ndawadzaza ndi mzimu waluso, kuti amsokere Aroni zobvala apatulidwe nazo, andicitire Ine nchito ya nsembe.

4. Ndipo zobvala azisoka ndizi: capacifuwa ndi efodi, ndi mwinjiro, ndi malaya opikapika, ndi nduwira, ndi mpango; tero apangire Aroni mbale wako ndi ana ace zobvala zopatulika, kuti andicitire Ine nchito ya nsembe,

5. Ndipo atenge golidi, ndi lamadzi ndi lofiirira ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa.

6. Naombe efodi ndi golidi, ndi lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira ndi bafuta wa thonje losansitsa, nchito ya mmisiri.

7. Akhale nazo zapamapewa ziwiri zomangika ku nsonga zace ziwiri, kuti amangike nazo.

8. Ndipo mpango wa efodi, wokhala pamenepo, kuti ammange nao, ukhale wa ciombedwe comweco, ndi woombera kumodzi, wagolidi, ndi thonje lamadzi, ndi lofiirira ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa.

9. Ndipo utenge miyala iwiri yaberulo, nulocepo maina a ana a Israyeli;

10. maina asanu ndi limodzi pa mwala wina, ndi maina asanu ndi limodzi otsala pa mwala unzace, mwa kubadwa kwao.

11. Uloce miyala iwiriyo ndi maina a ana a Israyeli, monga mwa nchito ya woloca miyala, monga malembedwe a cosindikizira, uipange igwirike ndi zoikamo zagolidi,

12. Ndipo ulike miyala iwiriyo pa zapamapewa za efodi, ikhale miyala ya cikumbutso ca ana a Israyeli; ndipo Aroni azinyamula maina ao pa mapewa ace awiri, akhale cikumbutso pamaso pa Yehova.

13. Ndipo upange zoikamo za golidi;

14. ndi maunyolo awiri a golidi woona; uwapote ngati zingwe, nchito yopota; numange maunyolo opotawo pazoikamo.

Werengani mutu wathunthu Eksodo 28