Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Eksodo 28:2-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

2. Ndipo usokere Aroni mbale wako zobvala zopatulika, zikhale zaulemerero ndi zokoma.

3. Ndipou lankhule ndi onse a mtima waluso, amene ndawadzaza ndi mzimu waluso, kuti amsokere Aroni zobvala apatulidwe nazo, andicitire Ine nchito ya nsembe.

4. Ndipo zobvala azisoka ndizi: capacifuwa ndi efodi, ndi mwinjiro, ndi malaya opikapika, ndi nduwira, ndi mpango; tero apangire Aroni mbale wako ndi ana ace zobvala zopatulika, kuti andicitire Ine nchito ya nsembe,

5. Ndipo atenge golidi, ndi lamadzi ndi lofiirira ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa.

6. Naombe efodi ndi golidi, ndi lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira ndi bafuta wa thonje losansitsa, nchito ya mmisiri.

7. Akhale nazo zapamapewa ziwiri zomangika ku nsonga zace ziwiri, kuti amangike nazo.

8. Ndipo mpango wa efodi, wokhala pamenepo, kuti ammange nao, ukhale wa ciombedwe comweco, ndi woombera kumodzi, wagolidi, ndi thonje lamadzi, ndi lofiirira ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa.

9. Ndipo utenge miyala iwiri yaberulo, nulocepo maina a ana a Israyeli;

10. maina asanu ndi limodzi pa mwala wina, ndi maina asanu ndi limodzi otsala pa mwala unzace, mwa kubadwa kwao.

Werengani mutu wathunthu Eksodo 28