Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Eksodo 28:17-27 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

17. Ndipo uikepo miyala yoikikapo, mizere inai ya miyala; mzere wa odemu, pitida, ndi bareketi, ndiyo ya mzere woyamba;

18. ndi mzere waciwiri wa nofeki, safiri, ndi yahaloni;

19. ndi mizere wacitatu wa lesemu, sibu, ndi akalama;

20. ndi mzere wacinai wa tarisisi, sohamu, ndi yasefe; zikhale zogwirika ndi golidi m'zoikamo zao.

21. Ndi miyalayi ikhale monga mwa maina a ana a Israyeli, khumindiawiri, monga maina ao; monga malocedwe a cosindikizira, yonse ikhale monga maina ao, kwa mafuko khumi ndi awiri.

22. Upangenso maunyolo pa capacifuwa ngati zingwe, nchito yopota, ya golidi woona.

23. Nupangire pa capacifuwa mphete ziwiri zagolidi, ndi kuzika mphete ziwirizo pa nsonga zace ziwiri za capacifuwa.

24. Numange maunyolo awiri opota agolidi ku mphete ziwiri pansonga pace pa capacifuwa.

25. Koma nsonga zace ziwiri za maunyolo opotawo uzimange ku zoikamo ziwiri, ndi kuziika pa zapamapewa ziwiri za efodi, m'tsogolo mwace.

26. Ndipo upange mphete ziwiri zagolidi, ndi kuzimanga pa nsonga zace ziwiri za capacifuwa, m'mphepete mwace, m katimo ku mbali ya kuefodi.

27. Upangenso mphete ziwiri zagolidi, ndi kuzimanga pa zapamapewa ziwiri za efodi, m'munsi, ku mbali yace ya kutsogolo, pafupi pa msoko wace, pamwamba pa mpango wa efodi.

Werengani mutu wathunthu Eksodo 28