Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Eksodo 27:8-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

8. Ulipange lagweregwere ndi matabwa; monga anakuonetsa m'phirimo; alipange momwemo.

9. Upangenso bwalo la cihema; pa mbali yace ya kumwela, kumwela, pakhale nsaru zocingira zakubwaloza nsaru ya bafuta wa thonje losansitsa, utali wace wa pa mbali imodzi mikono zana;

10. ndi nsici zace makumi awiri, ndi makamwa ao makumi awiri akhale amkuwa; zokowera za nsici ndi mitanda yace zikhale zasiliva.

11. Momwemonso pa mbali ya kumpoto m'utali mwace pakhale nsaru zocingira za mikono zana limodzi m'utali mwace; ndi nsici zace makumi awiri, ndi makamwa ao akhale amkuwa; zokowera za nsicizo ndi mitanda yace zikhale zasiliva.

12. Ndipo m'kupingasa kwa bwaloli pa mbali ya kumadzulo mukhale nsaru zocingira za mikono makumi asanu; nsici zace zikhale khumi, ndi makamwa ao khumi.

13. Ndipo m'kupingasa kwace kwa bwalo pa mbali ya kum'mawa, kum'mawa, mukhale mikono makumi asanu.

14. Ndi nsaru zocingira za pa mbali imodzi ya kucipata zikhale za mikono khumi ndi isanu; nsici zace zikhale zitatu, ndi makamwa ao atatu.

15. Ndi pa mbali yina pakhale nsaru zocingira za mikono khumi ndi isanu; nsici zace zikhale zitatu, ndi makamwa ao atatu.

16. Ndipo pa cipata ca bwalolo pakhale nsaru yotsekera ya mikono makumi awiri, ya lamadzi ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa, nchito ya wopikula; nsici zace zikhale zinai, ndi makamwa ao anai.

17. Nsici zonse za pabwalo pozungulira zimangike pamodzi ndi mitanda yasiliva; zokowera zao zasiliva, ndi makamwa ao amkuwa.

18. Utali wace wa bwalolo ukhale wa mikono zana limodzi, ndi kupingasa kwace makumi asanu monsemo, ndi msinkhu wace wa mpanda mikono isanu; ukhale wabafuta wa thonje losansitsa; ndi makamwa a nsicizo akhale amkuwa.

19. Zipangizo zonse za kacisi, m'macitidwe ace onse, ndi ziciri zace zonse, ndi ziciri zonse za bwalo lace, zikhale zamkuwa.

20. Ndipo uuze ana a Israyeli akutengere mafuta a azitona oyera opera akuunikira, kuti awalitse nyali kosalekeza.

21. Aroni ndi ana ace aikonze m'cihema cokomanako, kunja kwa nsaru yocinga yokhala kumboni, kuyambira madzulo kufikira m'mawa; likhale lemba losatha mwa mibadwo yao, alisunge ana a Israyeli.

Werengani mutu wathunthu Eksodo 27