Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Eksodo 27:3-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

3. Ndipo uzipanga zotayira zace zakulandira mapulusa ace, ndi zoolera zace, ndi mbale zowazira zace, ndi mitungo yace, ndi zoparira moto zace; zipangizo zace zonse uzipanga zamkuwa.

4. Ndipo ulipangire made, malukidwe ace ndi amkuwa; nupange pa malukidwewo ngondya zace zinai mphete zinai zamkuwa.

5. Nuwaike pansi pa matso a guwa la nsembelo posungulira, kuti malukidwe alekeze pakati pa guwa la nsembelo.

6. Ndipo upangire guwa la nsembe mphiko, mphiko za mtengo wasitimu, ndi kuzikuta ndi mkuwa.

7. Ndipo apise mphiko m'mphetezo kuti mphikozo zikhale pa mbali ziwiri za guwa la nsembe polinyamula.

8. Ulipange lagweregwere ndi matabwa; monga anakuonetsa m'phirimo; alipange momwemo.

9. Upangenso bwalo la cihema; pa mbali yace ya kumwela, kumwela, pakhale nsaru zocingira zakubwaloza nsaru ya bafuta wa thonje losansitsa, utali wace wa pa mbali imodzi mikono zana;

10. ndi nsici zace makumi awiri, ndi makamwa ao makumi awiri akhale amkuwa; zokowera za nsici ndi mitanda yace zikhale zasiliva.

11. Momwemonso pa mbali ya kumpoto m'utali mwace pakhale nsaru zocingira za mikono zana limodzi m'utali mwace; ndi nsici zace makumi awiri, ndi makamwa ao akhale amkuwa; zokowera za nsicizo ndi mitanda yace zikhale zasiliva.

12. Ndipo m'kupingasa kwa bwaloli pa mbali ya kumadzulo mukhale nsaru zocingira za mikono makumi asanu; nsici zace zikhale khumi, ndi makamwa ao khumi.

Werengani mutu wathunthu Eksodo 27