1. Ndipo uzipanga kacisi ndi nsaru zophimba khumi, za bafuta wa thonje losansitsa, ndi thonje lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira; uombemo akerubi, nchito ya mmisiri.
2. Utali wace wa nsaru yophimba imodzi ndiwo mikono makumi awiri kudza isanu ndi itatu, ndi kupingasa kwa nsaru imodzi ndiko mikono inai; nsaru zonse zikhale za muyeso umodzi.
3. Nsaru zisanu zilumikizane yina ndi inzace; ndi nsaru zisanu zina zilumikizane yina ndi inzace.
4. Ndipo uziika magango a nsaru yamadzi m'mphepete mwace mwa nsaru imodzi, ku mkawo wa cilumikizano; nucite momwemo m'mphepete mwace mwa nsaru ya kuthungoya cilumikizano dna.
5. Uziika magango makumi asanu pa nsaru yocingira imodzi, nuikenso magango makumi asanu m'mphepete mwace mwa nsaru ya cilumikizano cina; ndipo magango akomanizane lina ndi linzace.
6. Uzipanganso zokowera makumi asanu zagolidi, ndi kumanga nsaruzo pamodzi ndi zokowerazo; kuti kacisi akhale mmodzi.
7. Ndipo uziomba nsaru zophimba za ubweya wa mbuzi zikhale hema pamwamba pa kacisi; uziomba nsaru khumi ndi imodzi.
8. Utali wace wa nsaru imodzi ndiwo mikono makumi atatu, ndi kupingasa kwace kwa nsaru imodzi ndiko mikono inai; nsarukhumi ndi imodzi zikhale za muyeso womwewo.
9. Nuzisoka pamodzi nsaru zisanu pa zokha ndi nsaru zisanu ndi imodzi pa zokha, nupinde nsaru yacisanu ndi cimodziyo pa khomo la hema.