Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Eksodo 24:1-6 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo iye ananena ndi Mose, Ukwere kudza kwa Yehova, iwe ndi Aroni, Nadabu ndi Abihu, ndi akuru a Israyeli makumi asanu ndi awiri; ndipo mugwadire pakudza kutali;

2. ndipo Mose yekha ayandikire kwa Yehova; koma asayandikire iwowa; ndi anthunso asakwere naye.

3. Ndipo Mose anadza nafotokozera anthu mau onse a Yehova, ndi masveruzo onse; ndipo anthu onse anabvomera pamodzi, nati, Mau onse walankhula Yehova tidzacita.

4. Ndipo Mose analembera mau onse a Yehova, nalawira kuuka mamawa, namanga guwa la nsembe patsinde pa phiri, ndi zoimiritsa khumi ndi ziwiri, kwa mafuko khumi ndi awiri a Israyeli.

5. Ndipo anatuma ana a Israyeli a misinkhu ya anyamata, ndiwo anapereka nsembe zopsereza, naphera Yehova nsembe zamtendere, zang'ombe.

6. Ndipo Mose anagawa mwaziwo, nathira wina m'zotengera, nawaza wina pa guwa la nsembe.

Werengani mutu wathunthu Eksodo 24