Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Eksodo 23:6-15 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Usakhotetsa mlandu wa mnzako waumphawi.

7. Uzikhala kutali ndi mlandu wonama; ndipo usapha munthu wosacimwa ndi wolungama; pakuti sindidzayesa wolungama munthu woipa.

8. Usalandira cokometsera mlandu; pakuti cokometsera mlandu cidetsa maso a openya, nicisanduliza mlandu wa olungama,

9. Usampsinia mlendo; pakuti mudziwa mtima wa mlendo popeza munali alendo m'dziko la Aigupto.

10. Ndipo uzibzala m'munda mwako zaka zisanu ndi cimodzi, ndi kututa zipatso zako;

11. koma caka cacisanu ndi ciwiri uuleke, ugone; kuti aumphawi a anthu a mtundu wako adyemo ndipo zotsalira iwowa zoweta za kubusa zizidye; momwemo uzicita ndi munda wako wamphesa, ndimundawakowaazitona.

12. Uzicita nchito yako masiku asanu ndi limodzi, koma tsiku lacisanu ndi ciwiri uzipumula; kuti ng'ombe yako ndi buru wako zipumule, ndi kuti mwana wa mdzakaziwako ndi mlendo atsitsimuke.

13. Ndipo samalirani zonse ndanena ndi inu; nimusachule dzina la milungu yina; lisamveke pakamwa pako.

14. Muzindicitira loe madyerero katatu m'caka.

15. Uzisunga madyerero a mkate wopanda cotupitsa; masiku asanu ndi awiri uzidya mkate wopanda cotupitsa, monga ndinakuuza, nyengo yoikika, mwezi wa Abibu, pakuti m'menemo unaturuka m'Aigupto; koma asaoneke munthu pamaso panga opanda kanthu;

Werengani mutu wathunthu Eksodo 23