Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Eksodo 23:12-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. Uzicita nchito yako masiku asanu ndi limodzi, koma tsiku lacisanu ndi ciwiri uzipumula; kuti ng'ombe yako ndi buru wako zipumule, ndi kuti mwana wa mdzakaziwako ndi mlendo atsitsimuke.

13. Ndipo samalirani zonse ndanena ndi inu; nimusachule dzina la milungu yina; lisamveke pakamwa pako.

14. Muzindicitira loe madyerero katatu m'caka.

15. Uzisunga madyerero a mkate wopanda cotupitsa; masiku asanu ndi awiri uzidya mkate wopanda cotupitsa, monga ndinakuuza, nyengo yoikika, mwezi wa Abibu, pakuti m'menemo unaturuka m'Aigupto; koma asaoneke munthu pamaso panga opanda kanthu;

16. ndi madyerero a masika, zipatso zoyamba za nchito zako, zimene udazibzala m'munda; ndi madyerero a kututa, pakutha caka, pamene ututa nchito zako za m'munda.

17. Katatu m'caka amuna onse azioneka pamaso pa Ambuye Yehova.

18. Usapereka mwazi wa nsembe yanga pamodzi ndi mkate wacotupitsa; ndi mafuta a madyerero anga asagonamo kufikira m'mawa.

Werengani mutu wathunthu Eksodo 23