Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Eksodo 23:1-17 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Usatola mbiri yopanda pace; usathandizana naye woipa ndi kukhala mboni yocititsa ciwawa.

2. Usatsata unyinji wa anthu kucita coipa; kapena usacita umboni kumlandu, ndi kupatukira kutsata unyinji ndi kukhotetsa mlandu;

3. kapena usakometsera munthu wosauka pa mlandu wace.

4. Ukakomana ndi ng'ombe kapena buru wa mdani wako zirimkusokera, uzimbwezera izo ndithu.

5. Ukaona buru wa munthuwakudana nawe alikugona pansi ndi katundu wace, ndipo ukadaleka kuthandiza, koma uzimthandiza ndithu.

6. Usakhotetsa mlandu wa mnzako waumphawi.

7. Uzikhala kutali ndi mlandu wonama; ndipo usapha munthu wosacimwa ndi wolungama; pakuti sindidzayesa wolungama munthu woipa.

8. Usalandira cokometsera mlandu; pakuti cokometsera mlandu cidetsa maso a openya, nicisanduliza mlandu wa olungama,

9. Usampsinia mlendo; pakuti mudziwa mtima wa mlendo popeza munali alendo m'dziko la Aigupto.

10. Ndipo uzibzala m'munda mwako zaka zisanu ndi cimodzi, ndi kututa zipatso zako;

11. koma caka cacisanu ndi ciwiri uuleke, ugone; kuti aumphawi a anthu a mtundu wako adyemo ndipo zotsalira iwowa zoweta za kubusa zizidye; momwemo uzicita ndi munda wako wamphesa, ndimundawakowaazitona.

12. Uzicita nchito yako masiku asanu ndi limodzi, koma tsiku lacisanu ndi ciwiri uzipumula; kuti ng'ombe yako ndi buru wako zipumule, ndi kuti mwana wa mdzakaziwako ndi mlendo atsitsimuke.

13. Ndipo samalirani zonse ndanena ndi inu; nimusachule dzina la milungu yina; lisamveke pakamwa pako.

14. Muzindicitira loe madyerero katatu m'caka.

15. Uzisunga madyerero a mkate wopanda cotupitsa; masiku asanu ndi awiri uzidya mkate wopanda cotupitsa, monga ndinakuuza, nyengo yoikika, mwezi wa Abibu, pakuti m'menemo unaturuka m'Aigupto; koma asaoneke munthu pamaso panga opanda kanthu;

16. ndi madyerero a masika, zipatso zoyamba za nchito zako, zimene udazibzala m'munda; ndi madyerero a kututa, pakutha caka, pamene ututa nchito zako za m'munda.

17. Katatu m'caka amuna onse azioneka pamaso pa Ambuye Yehova.

Werengani mutu wathunthu Eksodo 23