Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Eksodo 22:4-19 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

4. Akacipeza cakubaco ciri m'dzanja lace camoyo, ngakhale ng'ombe, kapena buru, kapena nkhosa, alipe mowirikiza.

5. Munthu akadyetsa coweta pabusa kapena pa munda wamphesa, atamasula coweta cace, ndipo citadya podyetsa pa mwini wace; alipe podyetsa pace poposa, ndi munda wa mphesa wace woposa.

6. Ukayaka moto, nukalandira kuminga, kotero kuti unyeketsa mulu wa tirigu, kapena tirigu wosasenga, kapena munda; woyatsa motoyo alipe ndithu.

7. Munthu akaikiza ndalama kapena cuma kwa mnansi wace, ndipo zibeka m'nyumba ya munthuyo; akapeza mbala, ilipe cowirikiza.

8. Akapanda kumpeza mbalayo, abwere naye mwini nyumbayo kwa oweruza, kumuyesa ngati anaika dzanja lace pa cuma ca mnansi wace.

9. Mlandu uti wonse wa colakwa, kunena za ng'ombe, za buru, za nkhosa, za cobvala, za kanthu kali konse kotayika, munthu anenako kali kace; mlandu wa onse awiri ufike kwa oweruza; iye amene oweruza amtsutsa alipe cowirikiza kwa mnansi wace.

10. Munthu akaikiza buru, kapena ng'ombe, kapena nkhosa, kapena coweta cina kwa mnansi wace, ndipo cikafa, kapena ciphwetekwa, kapena wina acipitikitsa osaciona munthu;

11. lumbiro la Yehova likhale pakati pa iwo awiri, kuti sanaturutsa dzanja lace pa cuma ca mnansi wace; ndipo mwiniyo azibvomereza, ndipo asalipe.

12. Koma ngati cidabedwa kwaoko ndithu, alipe kwa mwiniyo.

13. Ngati cajiwa ndithu, abwere naco cikhale mboni; asalipe pa cojiwaco.

14. Munthu akabwereka cinthu kwa mnansi wace, ndipo ciphwetekwa, kapena cifa, mwiniyo palibe, azilipa ndithu.

15. Akakhalapo mwiniyo, asalipe; ngati cagwirira nchito yakulipira, cadzera kulipira kwace.

16. Munthu akanyenga namwali wosapalidwa ubwenzi, nakagona nave, alipetu kuti akhale mkazi wace.

17. Atate wace akakana konse kumpatsa iye, alipe ndalama monga mwa colipa ca anamwali.

18. Wanyanga usamlola akhale ndi moyo.

19. Ali yense agona ndi coweta aphedwe ndithu.

Werengani mutu wathunthu Eksodo 22