Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Eksodo 21:28-36 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

28. Ng'ombe ikatunga mwamuna kapena mkazi, nafa, aiponyetu miyala ng'ombeyo, osadya nyama yace; koma mwini ng'ombeyo azimasuka.

29. Koma ngati ng'ombe ikatunga masiku adapitawo, ndipo anamcenjeza mwiniyo, koma osaisunga iye, ndipo ikapha mwamuna kapena mkazi, aiponye miyala ng'ombeyo, ndi mwini waceyo amuphenso.

30. Akamuikira dipo, azipereka ciombolo ca moyo wace monga mwa zonse adamuikira.

31. Ingakhale yatunga mwana wamwamuna kapena wamkazi, aicitire monga mwa ciweruzo ici.

32. Ng'ombeyo ikatunga mnyamata kapena mdzakazi, azipatsa mbuye wace ndalama za masekele a siliva makumi atatu, ndipo ng'ombeyo aiponye miyala.

33. Munthu akafukula dzenje, kapena akakumba dzenje, osalibvundikira, ndipo ikagwamo ng'ombe kapena buru,

34. mwini dzenje azilipa; azilipa ndalama kwa mwini nyamayo, koma yakufayo ndi yace.

35. Ng'ombe ya mwini ikapweteka ng'ombe ya mnzace, nifa, azigulitsa ng'ombe yamoyoyo, nagawe ndalama zace; naigawe, ndi yakufa yomweyo.

36. Kapena kudadziwika kuti ng'ombeyo ikatunga masiku adapitawo, koma osaisunga mwiniyo, azilipa ndithu, ng'ombe kulipa ng'ombe, koma yakufayo ndi yace.

Werengani mutu wathunthu Eksodo 21