Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Eksodo 20:9-19 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. Masiku asanu ndi limodzi uzigwira, ndi kumariza nchito zako zonse;

10. koma tsiku lacisanu ndi ciwiri ndilo Sabata la Yehova Mulungu wako; usagwire nchito iri yonse, kapena iwe wekha, kapena mwana wako wamwamuna, kapena mwana wako wamkazi, kapena wanchito wako wamwamuna, kapena wanchito wako wamkazi, kapena nyama zako, kapena mlendo amene ali m'mudzi mwako;

11. cifukwa masiku asanu ndi limodzi Yehova adamariza zakumwamba ndi zapansi, ndi nyanja, ndi zinthu zonse ziri m'menemo, napumula tsiku ladsanu ndi ciwiri; cifukwa cace Yehova anadalitsa tsiku la Sabata kuti likhale lopatulika.

12. Uzilemekeza atate wako ndi amako; kuti acuruke masiku ako m'dziko limene Yehova Mulungu wako akupatsa iwe.

13. Usaphe.

14. Usacite cigololo.

15. Usabe.

16. Usamnamizire mnzako.

17. Usasirire nyumba yace ya mnzako, usasirire mkazi wace wa mnzako, kapena wanchito wace wamwamuna, kapena wanchito wace wamkazi, kapena ng'ombe yace, kapena buru wace, kapena kanthu kali konse ka mnzako.

18. Ndipo anthu onse anaona mabingu ndi zimphezi, ndi liu la lipenga, ndi phiri lirikufuka; ndipo pamene anthu anaziona, ananjenjemera, naima patali.

19. Ndipo anati kwa Mose, Mulankhule nafe ndinu, ndipo tidzamva; koma asalankhule nafe Mulungu, kuti tingafe,

Werengani mutu wathunthu Eksodo 20