Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Eksodo 18:1-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo Yetero, wansembe wa Midyani, mpongozi wa Mose, anamva zonse zimene Mulungu adacitira Mose ndi Israyeli anthu ace, kuti Yehova adaturutsa Israyeli m'Aigupto.

2. Ndipo Yetero, mpongozi wa Mose, anabwera naye Zipora mkazi wa Mose (atamtuma kwao), ndi ana ace awiri;

3. dzina la winayo ndiye Gerisomu, pakuti anati, Ndakhala mlendo m'dziko lacilendo;

4. ndi dzina la mnzace ndiye Eliezere; pakuti anati, Mulungu wa kholo langa anakhala thandizo langa nandilanditsa ku lupanga la Farao.

5. Ndipo Yetero, mpongozi wa Mose, anadza ndi ana ace amuna ndi mkazi wace kwa Mose kucipululu kumene adamangako, pa phiri la Mulungu;

6. nati kwa Mose, Ine mpongozi wako Yetero ndadza kwa iwe, ndi mkazi wako, ndi ana ace omwe awiri.

7. Ndipo Mose anaturuka kukakomana ndi mpongozi wace, nawerama, nampsompsona; nafunsana ali bwanji, nalowa m'hema.

8. Ndipo Mose anafotokozera mpongozi wace zonse Yehova adazicitira Farao ndi Aaigupto cifukwa ca Israyeli; ndi mabvuto onse anakomana nao panjira, ndi kuti Yehova adawalanditsa.

9. Ndipo Yetero anakondwera cifukwa ca zabwino zonse Yehova adazicitira Israyeli, ndi kuwalanditsa m'dzanja la Aaigupto.

10. Nati Yetero, Woyamikika Yehova, amene anakulanditsani m'dzanja la Aaigupto, ndi m'dzanja la Farao; ameneanalanditsa anthu awa pansi pa dzanja la Aaigupto.

11. Tsopano ndidziwa kuti Yehova ali wamkuru ndi milungu yonse; pakuti momwe anadzikuza okha momwemo anawaposa,

12. Ndipo Yetero, mpongozi wa Mose, anamtengera Mulungu nsembe Yopsereza, ndi nsembe zophera; ndipo Aroni ndi akuru onse a Israyeli anadza kudzadya mkate ndi mpongozi wa Mose pamaso pa Mulungu.

13. Ndipo kunatero kuti m'mawa mwace Mose anakhala pansi kuweruzira anthu mirandu yao; ndipo anthu anakhala ciriri pamaso pa Mose kuyambira m'mawa kufikira madzulo.

Werengani mutu wathunthu Eksodo 18