Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Eksodo 17:1-6 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo khamu lonse la ana a Israyeli linacoka m'cipululu ca Sini, m'zigono zao, monga mwa mau a Yehova, nagona m'Refidimu. Koma kumeneko kunalibe madzi akumwa anthu.

2. Pamenepo anthu anatsutsana ndi Mose, nati, Tipatseni madzi timwe, Koma Mose ananena nao, Mutsutsana nane bwanji? Muyeseranji Yehova?

3. Ndipo pomwepo anthu anamva ludzu lokhumba madzi; ndi anthu anadandaulira Mose, nati, Munatikwezeranji kucokera ku Aigupto, kudzatipha ife ndi ana athu ndi zoweta zathu ndi ludzu?

4. Ndipo Mose anapfuulira kwa Yehova, ndi kuti, Ndiwacitenji anthuwa? andilekera pang'ono kundiponya miyala.

5. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, Pita pamaso pa anthu, nutenge pamodzi nawe akuru ena a Israyeli; nutenge m'dzanja mwako ndodo ija unapanda nayo nyanja, numuke.

6. Taona, ndidzaima pamaso pako pathanthwe m'Horebe; ndipo upande thanthwe, nadzaturukamo madzi, kuti anthu amwe. Ndipo Mose anacita comweco pamaso pa akuru a Israyeli.

Werengani mutu wathunthu Eksodo 17