Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Eksodo 16:6-22 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Ndipo Mose ndi Aroni ananena ndi ana onse a Israyeli, Madzulo mudzadziwa kuti Yehova anakuturutsani m'dziko la Aigupto;

7. ndi m'mawa mwace mudzaona ulemerero wa Yehova, popeza alinkumva mulikudandaulira Yehova; pakuti ife ndife ciani, kuti mutidandaulira ife?

8. Nanenanso Mose, Pakukupatsani Yehova nyama ya kudya madzulo, ndi mkate wokhuta m'mawa, atero popeza Yehova adamva madandaulo anu amene mumdandaulira nao. Koma ife ndife ciani? simulikudandaulira ife koma Yehova.

9. Ndipo Mose anati kwa Aroni, Nena ndi khamu lonse la ana a Israyeli, Yandikizani pamaso pa Yehova, pakuti anamva madandaulo anu.

10. Ndipo kunakhala, pakunena Aroni ndi khamu lonse la ana a Israyeli kuti iwo anatembenukira kucipululu, ndipo, taonani, ulemerero wa Yehova unaoneka mumtambo.

11. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,

12. Ndamva madandaulo a ana a Israyeli; lankhula nao ndi kuti, Madzulo mudzadya nyama, ndi m'mawa mudzakhuta mkate; ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu.

13. Ndipo kunali madzulo zinakwera zinziri, ndipo zinakuta tsasa, ndi m'mawa padagwa mame pozungulira tsasa.

14. Ndipo atasansuka mame adagwawo, taonani, pankhope pa cipululu pali kanthu kakang'ono kamphumphu, kakang'ono ngati cipale panthaka.

15. Ndipo pamene ana a Israyeli anakaona, anati wina ndi mnzace, Nciani ici? pakuti sanadziwa ngati nciani. Ndipo Mose ananena nao, Ndiwo mkatewo Yehova wakupatsani ukhale cakudya canu,

16. Amenewo ndiwo mau walamulira Yehova, Aoleko yense monga mwa njala yace; munthu mmodzi omeri limodzi, monga momwe muli, yense atengere iwo m'hema mwace.

17. Ndipo ana a Israyeli anatero, naola wina wambiri, wina pang'ono.

18. Ndipo pamene anayesa ndi omeri, iye amene adaola wambiri sunamtsalira, ndi iye amene adaola pang'ono sunamsowa; yense anaola monga mwa njala yace.

19. Ndipo Mose ananena nao, Palibe munthu asiyeko kufikira m'mawa.

20. Koma sanammvera Mose; ndipo ena anasiyako kufikira m'mawa; koma unagwa mphutsi, nununkha. Ndipo Mose anakwiya nao.

21. Ndipo anauola m'mawa ndi m'mawa, yense monga mwa njala yace; popeza likatentha dzuwa umasungunuka.

22. Ndipo kunali tsiku lacisanu ndi cimodzi, anaola mkate, naonjezapo linzace, maomeri awiri pa munthu mmodzi; ndipo akazembe a khamulo anadza nauza Mose.

Werengani mutu wathunthu Eksodo 16