Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Eksodo 16:2-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

2. Ndipo khamu lonse la ana a Israyeli linadandaulira Mose ndi Aroni m'cipululu;

3. nanena nao ana a Israyeli, Ha! mwenzi titafa ndi dzanja la Yehova m'dziko la Aigupto, pokhala ife pa miphika ya nyama, pakudya mkate ife cokhuta; pakuti mwatiturutsa kudza nafe m'cipululu muno kudzapha msonkhano uwu wonse ndi njala.

4. Ndipo Yehova anati kwa Mose, Taona, ndidzabvumbitsira inu mkate wodzera kumwamba; ndipo anthu azituruka ndi kuola muyeso wa tsiku pa tsiku lace, kuti ndiwayese, ngati ayenda m'cilamulo canga kapena iai.

5. Ndipo kudzakhala tsiku lacisanu ndi cimodzi, kuti azikonza umene adabwera nao, ataoniezapo muyeso unzace wa pa tsiku limodzi.

6. Ndipo Mose ndi Aroni ananena ndi ana onse a Israyeli, Madzulo mudzadziwa kuti Yehova anakuturutsani m'dziko la Aigupto;

7. ndi m'mawa mwace mudzaona ulemerero wa Yehova, popeza alinkumva mulikudandaulira Yehova; pakuti ife ndife ciani, kuti mutidandaulira ife?

8. Nanenanso Mose, Pakukupatsani Yehova nyama ya kudya madzulo, ndi mkate wokhuta m'mawa, atero popeza Yehova adamva madandaulo anu amene mumdandaulira nao. Koma ife ndife ciani? simulikudandaulira ife koma Yehova.

9. Ndipo Mose anati kwa Aroni, Nena ndi khamu lonse la ana a Israyeli, Yandikizani pamaso pa Yehova, pakuti anamva madandaulo anu.

10. Ndipo kunakhala, pakunena Aroni ndi khamu lonse la ana a Israyeli kuti iwo anatembenukira kucipululu, ndipo, taonani, ulemerero wa Yehova unaoneka mumtambo.

11. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,

12. Ndamva madandaulo a ana a Israyeli; lankhula nao ndi kuti, Madzulo mudzadya nyama, ndi m'mawa mudzakhuta mkate; ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu.

13. Ndipo kunali madzulo zinakwera zinziri, ndipo zinakuta tsasa, ndi m'mawa padagwa mame pozungulira tsasa.

14. Ndipo atasansuka mame adagwawo, taonani, pankhope pa cipululu pali kanthu kakang'ono kamphumphu, kakang'ono ngati cipale panthaka.

15. Ndipo pamene ana a Israyeli anakaona, anati wina ndi mnzace, Nciani ici? pakuti sanadziwa ngati nciani. Ndipo Mose ananena nao, Ndiwo mkatewo Yehova wakupatsani ukhale cakudya canu,

16. Amenewo ndiwo mau walamulira Yehova, Aoleko yense monga mwa njala yace; munthu mmodzi omeri limodzi, monga momwe muli, yense atengere iwo m'hema mwace.

17. Ndipo ana a Israyeli anatero, naola wina wambiri, wina pang'ono.

18. Ndipo pamene anayesa ndi omeri, iye amene adaola wambiri sunamtsalira, ndi iye amene adaola pang'ono sunamsowa; yense anaola monga mwa njala yace.

Werengani mutu wathunthu Eksodo 16