Ndipo Yehova anati kwa Mose, Taona, ndidzabvumbitsira inu mkate wodzera kumwamba; ndipo anthu azituruka ndi kuola muyeso wa tsiku pa tsiku lace, kuti ndiwayese, ngati ayenda m'cilamulo canga kapena iai.