Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Eksodo 15:1-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Nyimbo yolemekeza Mulungu, Pamenepo Mose ndi ana a Israyeli anayimbira Yehova nyimbo iyi, nanena, ndi kuti,Ndidzayimbira Yehova pakuti wapambanatu;Kavalo ndi wokwera wace anawaponya m'nyanja.

2. Yehova ndiye mphamvu yanga ndi nyimbo yanga,Ndipo wakhala cipulumutso canga;Ameneyo ndiye Mulungu wanga, ndidzamlemekeza:Ndiye Mulungu wa kholo langa, ndidzammveketsa.

3. Yehova ndiye wankhondo;Dzina lace ndiye Yehova.

4. Magareta a Farao ndi nkhondo yace anawaponya m'nyanja;Ndi akazembe ace osankhika anamira m'Nyanja Yofiira.

5. Nyanja inawamiza:Anamira mozama ngati mwala.

6. Dzanja lanu lamanja, Yehova, lalemekezedwa ndi mphamvu,Dzanja lanu lamanja, Yehova, laphwanya mdani.

7. Ndipo ndi ukulu wanu waukuru mwapasula akuukira Inu;Mwatumiza mkwiyo wanu, unawanyeketsa ngati ciputu.

8. Ndipondi mpumo wa m'mphuno mwanu madzi anaunjikika,Mayendedwe ace anakhala ciriri ngati mulu;Zozama zinalimba m'kati mwa nyanja.

9. Mdani anati,Ndiwalondola, ndiwakumika, ndidzagawa zofunkha;Ndidzakhuta nao mtima;Ndidzasolola lupanga langa, dzanja langa lidzawaononga.

10. Munaombetsa mphepo yanu, nyanja inawamiza;Anamira m'madzi akuru ngati mtobvu.

11. Manana ndi Inu ndani mwa milungu, Yehova?Manana ndi Inu ndani, wolemekezedwa, woyera,Woopsa pomyamika, wakucita zozizwa?

12. Mwatambasula dzanja lanu lamanja,Nthaka inawameza,

13. Mwa cifundo canu mwatsogolera anthu amene mudawaombola;Mwa mphamvu yanu mudawalondolera njira yakumka pokhala panu poyera.

14. Mitundu ya anthu idamva, inanthunthumira;Kuda mtima kwagwira anthu okhala m'Filistiya.

Werengani mutu wathunthu Eksodo 15