Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Eksodo 13:12-22 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. kuti uzikapatulira Yehova onse oyamba kubadwa ndi oyamba onse uli nao odzera kwa zoweta; amunawo ndi a Yehova.

13. Koma woyamba yense wa buru uzimuombola ndi mwana wa nkhosa; ndipo ukapanda kumuombola uzimthyola khosi; koma oyamba onse a munthu mwa ana ako uziwaombola.

14. Ndipo kudzakhala, akakufunsa mwana wako masiku akudzawo ndi kuti, Ici nciani? ukanene naye, Yehova anatiturutsa m'Aigupto, m'nyumba ya aka polo, ndi dzanja lamphamvu;

15. ndipo kunakhala, pamene Farao anadziumitsa kuti tisamuke, Yehova anawapha onse oyamba kubadwa m'dziko la Aigupto, kuyambira oyamba a anthu, kufikira oyamba a zoweta; cifukwa cace ndimphera nsembe Yehova zazimuna zoyamba kubadwa zonse; koma oyamba onse a ana anga ndiwaombola.

16. Ndipo cizikhala ngati cizindikilo pa dzanja lako, ndi capamphumi pakati pa maso ako; pakuti Yehova anatiturutsa m'Aigupto ndi dzanja lamphamvu.

17. Ndipo kunakhala pamene Farao adalola anthu amuke, Mulungu sanawatsogolera njira ya dziko la Afilisti, ndiyo yaifupi; pakuti Mulungu anati. Angadodome anthuwo pakuona nkhondo ndi kubwerera m'mbuyo kumka ku Aigupto.

18. Koma Mulungu anawazungulitsa anthuwo, ku njira ya kucipululu ya Nyanja Yofiira; ndipo ana a Israyeli anakwera kucokera m'dziko la Aigupto okonzeka.

19. Ndipo Mose anamuka nao mafupa a Yosefe; pakuti adawalumbiritsatu ana a Israyeli ndi kuti, Mulungu adzakuzondani ndithu ndipo mukakwere nao mafupa anga osawwya kuno.

20. Ndipo anacokera ku Sukoti, nagona ku Etamu, pa malekezero a cipululu.

21. Ndipo Yehova anawatsogolera usana ndi mtambo njo kuwatsogolera m'njira; ndi usiku ndi moto njo, wakuwawalitsira; kuti ayende usana ndi usiku;

22. sanacotsa mtambo usana, kapena mtambo wamoto usiku, pamaso pa anthu.

Werengani mutu wathunthu Eksodo 13