Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Eksodo 13:1-7 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi kuti,

2. Ndipatulire Ine yense woyamba kubadwa, wotsegulira pa amace mwa ana a Israyeli, mwa anthu ndi mwa zoweta; ndiwo anga.

3. Ndipo Mose ananena ndi anthu, Kumbukirani tsiku linu limene munaturuka m'Aigupto, m'nyumba ya akapolo; pakuti Yehova anakuturutsani muno ndi dzanja lamphamvu; ndipo asadye kanthu ka cotupitsa.

4. Muturuka lero lino mwezi wa Abibu.

5. Ndipo kudzakhala atakulowetsa Yehova m'dziko la Akanani, ndi la Ahiti, ndi la Aamori ndi la Ahivi, ndi la Ayebusi, limene analumbira ndi makolo ako kukupatsa, m'dziko moyenda mkaka ndi uci ngati madzi, uzikasunga kutumikira kumeneku mwezi uno.

6. Masiku asanu ndi awiri uzikadya mkate wopanda cotupitsa, ndipo tsiku lacisanu ndi ciwiri likhale la madyerero a Yehova.

7. Azikadya mkate wopanda cotupitsa masiku asanu ndi awiriwo ndipo kasaoneke kanthu ka cotupitsa kwanu; inde cotupitsa cisaoneke kwanu m'malire ako onse.

Werengani mutu wathunthu Eksodo 13