37. Ndipo ana a Israyeli anayenda ulendo wakucokera ku Ramese kufikira ku Sukoti, zikwi mazana asanu ndi limodzi oyenda okha, ndiwo amuna, osawerenga ana.
38. Ndipo anthu ambiri osokonezeka anakwera nao; ndi nkhosa ndi ng'ombe, zoweta zambirimbiri.
39. Ndipo anaoca timitanda topanda cotupitsa ta mtanda umene anabwera nao ku Aigupto, popeza sadaikamo cotupitsa; pakuti adawapitikitsa ku Aigupto, ndipo sanathe kucedwa, kapena kudzikonzeratu kamba.
40. Ndipo kukhala kwa ana a Israyeli anakhala m'Aigupto ndiko zaka mazana anai kudza makumi atatu.
41. Ndipo kunakhala pakutha zaka mazana anai kudza makumi atatu, inde panakhala tsiku lomwelo, makamu onse a Yehova anaturuka m'dziko la Aigupto.
42. Ndiwo usiku wosungira Yehova ndithu, cifukwa ca kuwaturutsa m'dziko la Aigupto; usiku womwe uno ukhale wosungira Yehova ana onse a Israyeli ku mibadwo yao.
43. Ndipo Yehova anati kwa Mose ndi Aroni, Lemba la Paskha ndi ili: mwana wa mlendo ali yense asadyeko;
44. koma kapolo wa mwini ali yense, wogula ndi ndarama, utamdula, ndipo adyeko.
45. Mlendo kapena wolembedwa nchito asadyeko.
46. Audye m'nyumba imodzi; usaturukira nayo kubwalo nyama yina; ndipo musathyole pfupa lace.
47. Msonkhano wonse wa Israyeli uzicita ici.
48. Koma akakhala nanu mlendo, nakonzera Yehova Paskha, adulidwe amuna ace onse, ndipo pamenepo asendere kuucita; nakhale ngati wobadwa m'dziko; koma wosadulidwa ali yense asadyeko.