32. Muka nazoni zoweta zanu zazing'ono ndi zazikuru, monga mwanena; cokani, ndi kundidalitsa Inenso.
33. Ndipo Aaigupto anaumiriza anthuwo, nafulumira kuwaturutsa m'dziko; pakuti anati, Tiri akufa tonse.
34. Ndipo anthu anatenga mtanda wao usanatupe, ndi zoumbiramo zao zomangidwa m'zobvala zao pa mapewa ao.
35. Ndipo ana a Israyeli anacita monga mwa mau a Mose; napempha Aaigupto zokometsera zasiliva, ndi zagolidi, ndi zobvala.
36. Ndipo Yehova anapatsa anthu cisomo pamaso pa Aaigupto, ndipo sanawakaniza. Ndipo anawafunkhira Aaigupto.
37. Ndipo ana a Israyeli anayenda ulendo wakucokera ku Ramese kufikira ku Sukoti, zikwi mazana asanu ndi limodzi oyenda okha, ndiwo amuna, osawerenga ana.
38. Ndipo anthu ambiri osokonezeka anakwera nao; ndi nkhosa ndi ng'ombe, zoweta zambirimbiri.
39. Ndipo anaoca timitanda topanda cotupitsa ta mtanda umene anabwera nao ku Aigupto, popeza sadaikamo cotupitsa; pakuti adawapitikitsa ku Aigupto, ndipo sanathe kucedwa, kapena kudzikonzeratu kamba.
40. Ndipo kukhala kwa ana a Israyeli anakhala m'Aigupto ndiko zaka mazana anai kudza makumi atatu.
41. Ndipo kunakhala pakutha zaka mazana anai kudza makumi atatu, inde panakhala tsiku lomwelo, makamu onse a Yehova anaturuka m'dziko la Aigupto.
42. Ndiwo usiku wosungira Yehova ndithu, cifukwa ca kuwaturutsa m'dziko la Aigupto; usiku womwe uno ukhale wosungira Yehova ana onse a Israyeli ku mibadwo yao.