Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Eksodo 12:23-37 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

23. Pakuti Yehova adzapita pakatipo kukantha Aaigupto; koma pamene adzaona mwaziwo pa mphuthu pamwamba ndi za pambali, Yehova adzapitirira pakhomopo, osalola woonongaalowe m'nyumba zanu kukukanthani.

24. Ndipo muzisunga cinthu ici cikhale lemba la kwa inu, ndi kwa ana anu ku nthawi zonse.

25. Ndipo kudzakhala, pamene mulowa m'dziko limene Yehova adzakupatsani, mensa analankhula, muzisunga kutumikira kumeneku.

26. Ndipo kudzakhala, pamene ana anu adzanena ndi inu, Kutumikiraku muli nako nkutani?

27. mudzati, Ndiko nsembe ya Paskha wa Yehova, amene anapitirira nyumba za ana a Israyeli m'Aigupto, pamene anakantha Aaigupto, napulumutsa nyumba zathu.

28. Ndipo anthu anawerama, nalambira. Ndipo ana a Israyeli anamuka nacita monga Yehova adalamulira Mose ndi Aroni; anacita momwemo.

29. Ndipo panakhala pakati pa usiku, Yehova anakantha ana oyamba onse a m'dziko la Aigupto, kuyambira mwana woyamba wa Earao wakukhala pa mpando wacifumu wace kufikira mwana woyamba wa wam'nsinga ali m'kaidi; adi ana oyamba onse a zoweta.

30. Ndipo Farao anauka usiku, iyendi anyamata ace onse, ndi Aaigupto onse; ndipo kunali kulira kwakukulu m'Aigupto; pakuti panalibe nyumba yopanda wakufa m'mwemo.

31. Ndipo anaitana Mose ndi Aroni usiku, nati, Ukani, turukani pakati pa anthu anga, inu ndi ana a Israyeli; ndipo mukani katumikireni Yehova, monga mwanena.

32. Muka nazoni zoweta zanu zazing'ono ndi zazikuru, monga mwanena; cokani, ndi kundidalitsa Inenso.

33. Ndipo Aaigupto anaumiriza anthuwo, nafulumira kuwaturutsa m'dziko; pakuti anati, Tiri akufa tonse.

34. Ndipo anthu anatenga mtanda wao usanatupe, ndi zoumbiramo zao zomangidwa m'zobvala zao pa mapewa ao.

35. Ndipo ana a Israyeli anacita monga mwa mau a Mose; napempha Aaigupto zokometsera zasiliva, ndi zagolidi, ndi zobvala.

36. Ndipo Yehova anapatsa anthu cisomo pamaso pa Aaigupto, ndipo sanawakaniza. Ndipo anawafunkhira Aaigupto.

37. Ndipo ana a Israyeli anayenda ulendo wakucokera ku Ramese kufikira ku Sukoti, zikwi mazana asanu ndi limodzi oyenda okha, ndiwo amuna, osawerenga ana.

Werengani mutu wathunthu Eksodo 12