2. Mwezi uno uzikhala kwa inu woyamba wa miyezi; muziuyesa mwezi woyamba wa caka.
3. Mulankhule ndi msonkhano wonse wa Israyeli ndi kuti, Tsiku lakhumi la mwezi uno adzitengere munthu yense mwana wa nkhosa, monga mwa mabanja a atate ao, mwana wa nkhosa pabanja.
4. Banja likaperewera mwana wa nkhosa, munthu ndi mnzace ali pafupi pa nyumba yace atenge monga mwa kufikira kwa anthu ao; muziwerengera mwana wa nkhosa monga mwa kudya kwao.
5. Mwana wa nkhosa wanu azikhala wangwiro, wamwamuna, wa caka cimodzi; muzimtenga ku nkhosa kapena ku mbuzi.
6. Ndipo mukhale naye cisungire kufikira tsiku lakhumi ndi cinai la mwezi womwe; ndipo bungwe lonse la anthu a Israyeli lizimupha madzulo.
7. Ndipo azitengako mwazi, naupake pa mphuthu za mbali ndi ya pamwamba m'nyumba zimene adyeramo.
8. Ndipo azidya nyamayo usiku womwewo, yooca pamoto, ndi mkate wopanda cotupitsa; aidye ndi ndiwo zowawa,
9. Musaidya yaiwisi, kapena yophika ndi madzi konse ai, koma yooca pamoto; muti wace ndi miyendo yace ndi matumbo ace.
10. Ndipo musasiyako kufikira m'mawa; koma yotsalira kufikira m'mawayo muipsereze ndi moto:
11. Ndipo muziidya cotero: okwinda m'cuuno, nsapato zanu pa mapazi anu ndodo yanu m'dzanja lanu, ndipo muziidya msanga; ndiye Paskha wa Yehova.
12. Pakuti ndidzapita pakati pa dziko la Aigupto usiku womwewo, ndi kukantha ana oyamba onse m'dziko la Aigupto, anthu ndi zoweta; ndipo ndidzacita maweruzo pa milungu yonse ya Aigupto; Ine ndine Yehova.