Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Deuteronomo 6:18-24 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

18. Ndipo muzicita zolunjika ndi zokoma pamaso pa Yehova; kuti cikukomereni, ndi kuti mulowe kukalandira dziko lokomali Yehova analumbirira makolo anu,

19. kuingitsa adani anu onse pamaso panu, monga Yehova adanena.

20. Akakufunsani ana anu m'tsogolomo, ndi kuti, Mbonizo, ndi malemba, ndi maweruzo, zimene Yehova Mulungu wathu anakulamulirani, zitani?

21. Pamenepo muzinena kwa ana anu, Tinali akapolo a Farao m'Aigupto; ndipo Yehova anatiturutsa m'Aigupto ndi dzanja lamphamvu.

22. Ndipo Yehova anapatsa zizindikilo ndi zozizwa zazikuru ndi zowawa m'Aigupto, pa Farao, ndi pa nyumba yace yonse, pamaso pathu;

23. ndipo anatiturutsa komweko, kuti atilowetse, kutipatsa dzikoli analumbirira makolo athu.

24. Ndipo Yehova anatilamulira tizicita malemba awa onse, kuopa Yehova Mulungu wathu, kuti tipindule nako masiku onse, kuti atisunge amoyo, monga lero lino.

Werengani mutu wathunthu Deuteronomo 6