Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Deuteronomo 4:10-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. Tsikuli munaima pamaso pa Yehova Mulungu wanu m'Horebe muja Yehova anati kwa ine, Ndisonkhanitsire anthu, ndidzawamvetsa mau anga, kuti aphunzire kundiopa Ine masiku ao onse akukhala ndi moyo pa dziko lapansi, ndi kuti aphunzitse ana ao.

11. Ndipo munayandikiza ndi kuima patsinde pa phiri; ndi phizilo linayaka mota kufikira pakati pa thambo; kunali mdima, ndi mtambo, inde mdima bii.

12. Pamenepo Yehova ananena ndi inu ali pakati pa moto; munamva kunena kwa mau, osaona maonekedwe, koma kunenako.

13. Pamenepo anakufotokozerani cipangano cace, cimene anakulamulirani kucicita, ndiwo Mau Khumi; nawalemba pa magome awiri amiyala.

14. Ndipo Yehova anandilamulira muja ndikuphunzitseni malemba ndi maweruzo, kuti mukawacite m'dziko limene muolokerako kulilandira likhale lanu lanu.

15. Potero dzicenjerani nao moyo wanu ndithu; popeza simunapenya mafanidwe konse tsikuli Yehova ananena ndi inu m'Horebe, ali pakati pa moto;

16. kuti mungadziipse, ndi kudzipangira fano losema, lakunga cifaniziro ciri conse, mafanidwe a mwamuna kapena mkazi;

Werengani mutu wathunthu Deuteronomo 4